🌐 Language
'Olelo Hawai'iAfaan Oromoobahasa IndonesiaBelarusianBrezhonegCebuanoChamorroChichewachiShonaChongthuCiyawoDanskDeutschEestiEnglishEspañolEsperantoeʋegbeFrançaisHausaHrvatskiIgboIlocanoItalianoKikuyuKiswahiliKiyombiKreyòl AyisyenLatinaLatviešulietuviųLingálaLugandaMagyarMahasuiMāoriNederlandsNorskPohnpeianPolskiPortuguêsQach’abelRomaniRomânăSanskritSetswanaShqipsrpski jezikSuomiSvenskaTagalogTiếng ViệtTonganTwiTürkçeUyghur tiliYorùbáÍslenskaČeštinaБългарскиРусскийУкраїнськаעבריתاردوالعربيةفارسیكوردی سۆرانیअहिराणी‎नेपालीभद्रवाही‎मराठीमानक हिन्दी‎हरियाणवी‎অসমীয়াবাংলাਪੰਜਾਬੀગુજરાતીଓଡ଼ିଆ‎தமிழ்తెలుగుಕನ್ನಡമലയാളംไทยဗမာἙλληνική中文日本語한국어+ Zilankhulo zonse
See More Jesus
Chichewa

Kodi Baibulo Limanena Chiyani Za Kukhazikika? — Kuchiika M'ntchito · Malemba a KJV okhala ndi Manambala a Strong's — Mafunso a Baibulo

Mafunso a Baibulo

Kodi Baibulo Limanena Chiyani Za Kukhazikika? — Kuchiika M'ntchito · Malemba a KJV okhala ndi Manambala a Strong's — Mafunso a Baibulo

Pa lemba lililonse pansipa, sankhani chimene vesiyo limaphunzitsa. Zambiri zanu zidzaonekera kumapeto.

Awa ndi mayeso oyesedwa. Apambaneni kuti mupeze mfundo zopita ku Satifiketi ya Chivomerezo cha Utumiki yanu.

Ahebri 11:6 — Ndipo popanda chikhulupiriro nʼkosatheka kukondweretsa Mulungu, chifukwa aliyense amene amabwera kwa Iye ayenera kukhulupirira kuti Mulungu alipodi ndi kuti Iye amapereka ________ kwa amene akumufunitsitsa.
wosatha
utumiki
mphotho
Miyambo 11:27 — Iye amene amafunafuna zabwino mwakhama ________ zabwinozo, koma wofunafuna zoyipa zidzamupeza.
Amasunga
amapeza
amadana
Masalimo 63:1 — Inu Mulungu, ndinu Mulungu wanga, moona mtima ine ndimakufunafunani; moyo wanga uli ndi ludzu lofuna Inu, ________ langa likulakalaka inu, mʼdziko lowuma ndi lotopetsa kumene kulibe madzi.
thupi
yekha
ulemu
Masalimo 78:34 — Mulungu atawapha, iwo amamufunafuna Iyeyo; iwo ankatembenukiranso kwa Iye ________.
mwachangu
anatsogolera
kuwerengedwa
Miyambo 8:19 — Chipatso changa ndi chabwino kuposa golide, ngakhale golide wosalala; zimene ine ndimabereka zimaposa ________ wabwino kwambiri.
chisoni
siliva
mphatso
Deuteronomo 6:17 — Onetsetsani kuti mukusunga ________ a Yehova Mulungu wanu, malangizo ake ndi zikhazikitso zake zimene anakulamulirani.
mitundu
adani
malamulo
Deuteronomo 11:13 — Choncho mukasunga ________ malamulo amene ndikukupatsani lero lino, kukonda Yehova Mulungu wanu ndi kumutumikira Iyeyo ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse
mwachilungamo
zokoma
mokhulupirika
Yoswa 22:5 — Koma samalitsani kuti mumvere malamulo ndi malangizo amene Mose mtumiki wa Yehova anakupatsani: kukonda Yehova Mulungu wanu, kuchita zimene iye amafuna, ________ malamulo ake, kukhala okhulupirika kwa Iye ndi kumutumikira ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse.”
abwenzi
kumvera
ukali
Masalimo 119:4 — Inu mwapereka ________ ndipo ayenera kutsatidwa kwathunthu.
kumene
njira
malangizo
Masalimo 119:2 — Odala ndi amene amasunga ________ ake, amene amafunafuna Iyeyo ndi mtima wawo wonse.
ulemerero
malamulo
adani
Mlaliki 9:10 — Ntchito iliyonse imene ukuyigwira, uyigwire ndi mphamvu zako zonse, pakuti ku ________ kumene ukupita kulibe kugwira ntchito, kulibe malingaliro, chidziwitso ndiponso nzeru.
manda
oyamba
zikho
Miyambo 20:13 — Usakonde ________ ungasauke; khala maso ndipo udzakhala ndi chakudya chambiri.
tulo
mtengo
mphatso
2 Petro 1:5 — Choncho, chitani khama kuwonjezera moyo wabwino pa ________ chanu, ndipo pa moyo wabwino muwonjezerepo nzeru.
chikhulupiriro
chisomo
ulemu
1 Akorinto 15:58 — Choncho, abale anga ________ imani njii. Musasunthike ndi chilichonse. Nthawi zonse mudzipereke kwathunthu ku ntchito ya Ambuye, chifukwa mukudziwa kuti ntchito zanu mwa Ambuye sizili zopanda phindu.
okondedwa
mwamphamvu
posachedwapa
1 Timoteyo 6:12 — Menya nkhondo yabwino yachikhulupiriro. Gwiritsitsa moyo wosatha umene anakuyitanira pamene unavomereza bwino lomwe pamaso pa ________ zambiri.
mtumwi
chinsinsi
mboni
2 Timoteyo 2:3 — Umve nane zowawa, monga ________ wa Khristu Yesu.
msilikali
utumiki
Mlaliki
2 Timoteyo 2:4 — Palibe msilikali amene ali pa ntchito amagwiranso ntchito za anthu wamba, iye amafuna ________ bwana wolamulira.
kupitiriza
kukondweretsa
kulemekeza
Aefeso 6:11 — Valani zida zonse za Mulungu kuti muthe kuyima ndi kukana machenjerero a ________.
Satana
Paulo
Pilato
2 Akorinto 7:11 — Taonani zimene chisoni chimene Mulungu amafuna chatulutsa mwa inu. Chatulutsa khama lalikulu, chakuthandizani kuti mudzikonze nokha, chakukwiyitsani kwambiri, komanso chakupatsani mantha aakulu. Chakuchititsani kuti mufune kundiona ine, mwakhudzidwa kwambiri ndipo mukufuna kuonetsetsa kuti chilungamo chachitikadi. Pa ________ yonseyi, mwaonetsadi kuti ndinu osalakwa.
wosatha
nkhani
njala
2 Akorinto 8:16 — Tithokoze Mulungu amene anayika mu mtima wa ________ changu chomwecho chimene ine ndili nacho pa inu.
Makedoniya
Akaya
Tito
2 Akorinto 8:22 — Kuwonjezera apo, tikuwatumiza pamodzi ndi mʼbale wathu, amene nthawi zambiri watitsimikizira mʼnjira zosiyanasiyana kuti ndi ________ ndiponso chifukwa ali ndi chikhulupiriro chachikulu mwa inu.
tikufa
wathupi
wachangu
2 Timoteyo 1:17 — Mʼmalo mwake, atangofika ku ________, anandifunafuna ndipo anandipeza.
Trowa
Prisila
Roma
Machitidwe a Atumwi 17:11 — Tsopano anthu a ku Bereya anali akhalidwe labwino kusiyana ndi Atesalonika, pakuti iwo analandira mawu ndi chidwi chachikulu ndipo ankasanthula ________ tsiku ndi tsiku kuti aone ngati zimene ankanena Paulozo zinali zoona.
mtsikana
Malemba
anakumana
Luka 15:8 — “Kapena tiyeni tifanizire mayi amene anali ndi ndalama zasiliva khumi ndipo imodzi nʼkutayika, kodi sayatsa ________ ndi kusesa mʼnyumba ndi kufuna mosamalitsa mpaka atayipeza?
mbiri
Atate
nyale
Machitidwe a Atumwi 20:24 — Koma sindilabadira konse za moyo wanga ngati kuti ndi wa mtengo wapatali kwa ine, malingana ndikatsirize ntchito yanga ndi ________ umene Ambuye Yesu anandipatsa, ntchito yochitira umboni Uthenga Wabwino wachisomo cha Mulungu.
utumiki
kuchiritsa
dera
2 Timoteyo 4:5 — Koma iwe, khala tcheru nthawi zonse, pirira mʼzovuta, gwira ntchito ya ________, gwira ntchito zonse za utumiki wako.
kuphunzira
mlaliki
amoyo
Yakobo 1:12 — Wodala ndi munthu amene amapirira ________, chifukwa akapambana adzalandira chipewa cha ulemerero chimene Mulungu analonjeza anthu amene amamukonda.
chikhululukiro
kufatsa
mʼmayesero
Chivumbulutso 2:10 — Musachite mantha ndi zimene muti musauke nazo posachedwapa. Ndithu, ________ adzayika ena a inu mʼndende pofuna kukuyesani, ndipo mudzazunzika kwa masiku khumi. Khalani okhulupirika ngakhale zitafika pa imfa, ndipo Ine ndidzakupatsani chipewa cha ulemerero wamoyo.
Ziyoni
Pilato
Satana
2 Timoteyo 4:18 — Ambuye adzandilanditsa ku chilichonse chofuna kundichita choyipa ndipo adzandisamalira bwino mpaka kundilowetsa chonse mu ufumu wake ________. Kwa Iye kukhale ulemerero mpaka muyaya.
wakumwamba
mlandu
Kuyambira

← Bwererani ku phunziroli