Yeremiya 4:22 — Yehova akuti, “Anthu anga ndi ________; iwo sandidziwa. Iwo ndi ana opanda nzeru; samvetsa chilichonse. Ali ndi luso lochita zoyipa, koma sadziwa kuchita zabwino.”
zitsiru
njoka
mikango
Yeremiya 13:23 — Kodi wa dziko la Kusi nʼkusintha khungu lake, kapena ________ kusintha mawanga ake? Inunso amene munazolowera kuchita zoyipa simungathe kusintha.
mankhwala
kambuku
okonzekera
Miyambo 4:14 — Usayende mʼnjira za anthu ________ kapena kuyenda mʼnjira ya anthu ochimwa.
dzina
oyipa
bedi
Miyambo 4:18 — Koma njira ya anthu olungama ili ngati kuwala kwa mʼbandakucha kumene kumanka kuwalirawalira mpaka ________ litafika pa mutu.
Genesis 3:6 — Pamene mkaziyo anaona kuti mtengowo unali wabwino kudya ndi wokongola ndi kuti unali wopatsa nzeru, anatengako zipatso zake nadya. Zina anamupatsako ________ wake amene anali naye pomwepo ndipo naye anadyanso.
pangano
banja
mwamuna
Genesis 3:8 — Kenaka munthu uja ndi mkazi wake anamva mtswatswa wa Yehova Mulungu akuyendayenda mʼmundamo ________ a tsikulo, ndipo iwo anabisala pamaso pa Yehova Mulungu pakati pa mitengo ya mʼmundamo.
chisoni
wokongola
madzulo
Genesis 3:22 — Ndipo Yehova Mulungu anati, “Tsopano munthu uyu wasanduka mmodzi wa ife, wodziwa zabwino ndi zoyipa. Iyeyu asaloledwe kutambasula dzanja ndi kutengako ________ za mu mtengo wopatsa moyo uja kuti angakhale ndi moyo mpaka muyaya.”
woyamba
zipatso
mlendo
Genesis 8:20 — Pamenepo ________ anamanga guwa lansembe la Yehova ndipo anatengako mtundu uliwonse wa nyama zoti nʼkudya ndi mbalame zoti nʼkudya naperekapo nsembe yopsereza.
Metusela
Yaredi
Nowa
Miyambo 1:33 — Koma aliyense wondimvera adzakhala mwa ________; adzakhala mosatekeseka posaopa chilichonse.”
chilango
bata
wowukira
1 Petro 2:24 — Iye mwini anasenza machimo athu mʼthupi lake pa mtanda, kuti ife tife kutchimo ndi kukhala ndi moyo potsata chilungamo, ndipo ndi ________ ake munachiritsidwa.