Aefeso 1:7 — Mwa Yesu Khristu, chifukwa cha magazi ake, ife tinawomboledwa ndi kukhululukidwa machimo athu molingana ndi kuchuluka kwa ________ cha Mulungu
chiyembekezo
thupi
chisomo
Yohane 19:34 — Mʼmalo mwake, mmodzi wa asilikaliwo anamubaya Yesu ndi ________ mʼnthiti, ndipo nthawi yomweyo munatuluka magazi ndi madzi.
mkwati
Malemba
mkondo
Machitidwe a Atumwi 2:38 — Petro anawayankha kuti, “Lapani ndipo mubatizidwe aliyense wa inu, mʼdzina la Yesu Khristu kuti ________ anu akhululukidwe. Ndipo mudzalandira mphatso ya Mzimu Woyera.
machimo
mphamvu
moyo
Machitidwe a Atumwi 3:19 — Chifukwa chake, lapani, bwererani kwa Mulungu, kuti ________ anu afafanizidwe, kuti nthawi ya kutsitsimuka ibwere kuchokera kwa Ambuye
Machitidwe a Atumwi 22:16 — Ndipo tsopano ukudikira chiyani? Dzuka ndi kutama dzina la Ambuye mopemba, ubatizidwe ndi ________ machimo ako.’
kuchotsa
kuyamika
pafupifupi
Aroma 6:4 — Chifukwa chake ife tinayikidwa ________ pamodzi ndi Iye mwa ubatizo. Tinalowa mu imfa ndi cholinga choti monga momwe Khristu anaukitsidwa kwa akufa ndi ulemerero wa Atate, ifenso tikakhale mʼmoyo watsopano.
nyale
mʼmanda
mbiri
Akolose 2:12 — Mu ________, munayikidwa mʼmanda pamodzi ndi Khristu ndi kuukitsidwa naye pamodzi, pokhulupirira mphamvu za Mulungu amene anamuukitsa kwa akufa.
ubatizo
mtumwi
ngongole
1 Petro 3:21 — Madziwo akufanizira ubatizo umene lero ukukupulumutsaninso, osati chifukwa chochotsa litsiro la mʼthupi koma chifukwa cha ________ choona pamaso pa Mulungu. Umakupulumutsani chifukwa cha kuuka kwa Yesu Khristu
chikumbumtima
chipulumutso
mdima
Yohane 3:5 — Yesu anayankha kuti, “Zoonadi, Ine ndikukuwuza kuti ngati munthu sabadwa mwa madzi ndi ________ Woyera, sangalowe mu ufumu wa Mulungu.
Mzimu
yekha
ulemu
Agalatiya 3:27 — pakuti nonse amene munalumikizana ndi Khristu mu ________ munavala Khristu.
ubatizo
mipingo
kupembedza
2 Mafumu 5:14 — Choncho ________ anapita ku Yorodani nakadzimiza mʼmadzimo kasanu nʼkawiri, monga momwe munthu wa Mulungu anamuwuzira. Thupi lake linakhalanso monga kale ndipo linakhala losalala ngati la kamnyamata.
Yoramu
Naamani
Gehazi
Aefeso 1:13 — Ndipo inunso pamene munamva mawu a choonadi, Uthenga Wabwino wa ________ chanu, munayikidwanso mwa Khristu. Mutakhulupirira, anakusindikizani chizindikiro pokupatsani Mzimu Woyera amene Iye analonjeza.
malangizo
mdima
chipulumutso
1 Yohane 1:9 — Koma tikavomereza machimo athu, Iye ndi wokhulupirika ndi wolungama ndipo adzatikhululukira machimo athu, nadzatiyeretsa ndi kutichotsera ________ chilichonse.
kupembedzera
chikumbumtima
chosalungama
Yohane 15:4 — Khalani mwa Ine, monga Ine ndili mwa inu. Palibe nthambi imene ingabereke chipatso pa yokha ngati sinalumikizike ku ________. Chomwechonso inu simungathe kubereka chipatso pokhapokha mutakhala mwa Ine.
mpesa
tsitsi
ziwanda
Akolose 1:23 — ngati mupitirirabe kukhala mʼchikhulupiriro chanu, okhazikika ndi olimba, osasunthidwa kuchoka pa chiyembekezo chimene munachigwira mu Uthenga Wabwino. Uwu ndi Uthenga Wabwino umene munawumva, umene wakhala ukulalikidwa kwa olengedwa onse a pansi pa ________, ndi umenenso, ine Paulo ndinakhala mtumiki wake.
mwambo
thambo
abwenzi
Chivumbulutso 2:10 — Musachite mantha ndi zimene muti musauke nazo posachedwapa. Ndithu, Satana adzayika ena a inu mʼndende pofuna kukuyesani, ndipo mudzazunzika kwa masiku khumi. Khalani okhulupirika ngakhale zitafika pa imfa, ndipo Ine ndidzakupatsani ________ cha ulemerero wamoyo.
chipewa
fano
mwala
1 Yohane 2:1 — Inu Ana anga okondedwa, ndikukulemberani zimenezi kuti musachimwe. Koma wina akachimwa, tili nayo Nkhoswe yotinenera kwa ________, Yesu Khristu, Wolungamayo.
mlandu
makolo
Atate
Masalimo 103:12 — monga kummawa kutalikirana ndi kumadzulo, koteronso Iye watichotsera mphulupulu zathu kuti zikhale ________ nafe.