Kodi Yesu Ndani? — Gawo 2 · Malemba a KJV pamodzi ndi Manambala a Strong — Mafunso a Baibulo Pa lemba lililonse pansipa, sankhani chimene vesiyo limaphunzitsa. Zambiri zanu zidzaonekera kumapeto.
Awa ndi mayeso oyesedwa. Apambaneni kuti mupeze mfundo zopita ku Satifiketi ya Chivomerezo cha Utumiki yanu.
Zekariya 6:12 — Muwuze kuti zimene akunena Yehova Wamphamvuzonse ndi izi: ‘Taonani, munthu wotchedwa ________ ndi ameneyu, ndipo adzaphuka pomwe alipo ndi kumanga Nyumba ya Yehova.
Nthambi
chete
mtengo
Genesis 14:18 — Ndipo Melikizedeki mfumu ya ku ________ anabweretsa buledi ndi vinyo. Iyeyu anali wansembe wa Mulungu Wammwambamwamba
Gomeri
Salemu
Hava
Masalimo 110:4 — Yehova walumbira ndipo sadzasintha maganizo ake: “Ndiwe wansembe mpaka muyaya monga mwa unsembe wa ________.”
Zalimuna
Melikizedeki
Asikeloni
Ahebri 7:1 — Melikizedeki ameneyu anali mfumu ya ku ________, ndiponso wansembe wa Mulungu Wammwambamwamba. Anakumana ndi Abrahamu pamene ankabwerera kuchokera ku nkhondo atagonjetsa mafumu aja, Melikizedeki anakumana naye namudalitsa.
Italiya
Mateyu
Salemu
Ahebri 7:4 — Mukuona tsono kuti munthuyo anali wamkulu ndithu, pakuti Abrahamu kholo lathu anamupatsa ________ cha zimene anafunkha.
ochimwa
chakhumi
ulemerero
Ahebri 7:26 — Uyu ndi Mkulu wa ansembe amene tikumufuna chifukwa ndi woyera, wopanda choyipa kapena chodetsa chilichonse, wosiyana ndi anthu ________, ndiponso wokwezedwa kuposa zonse zakumwambaku.
malemba
ochimwa
mizimu
Mateyu 26:26 — Pamene ankadya, Yesu anatenga buledi, nayamika ndipo anamunyema nagawira ophunzira ake nanena kuti, “Tengani, idyani; ili ndi ________ langa.”
thupi
mneneri
kuposa
Genesis 49:10 — ________ yaufumu sidzachoka mwa Yuda, udzawupanirira ulamuliro motero kuti palibe amene adzawuchotse, mpaka mwini wake weniweni atabwera ndipo mitundu yonse ya anthu idzamumvera.
kumwa
Ndodo
nkhunda
Masalimo 132:11 — Yehova analumbira kwa Davide, lumbiro lotsimikizika kuti Iye sadzasintha: “Mmodzi wa ana ako ndidzamuyika pa mpando ________;
thupi
waufumu
pangano
Yeremiya 23:5 — Yehova akuti, “Masiku akubwera, pamene ndidzaphukitsira Davide ________ yowongoka. Imeneyi ndiye mfumu imene idzalamulira mwanzeru, mwachilungamo ndi mosakondera mʼdziko.
chigololo
chilungamo
Nthambi
Mateyu 1:1 — Buku lofotokoza za ________ wa Yesu Khristu mwana wa Davide, mwana wa Abrahamu:
ulamuliro
mʼbado
umboni
2 Timoteyo 2:8 — Kumbukira Yesu Khristu wochokera ku mtundu wa Davide kuti anauka kwa akufa. Uwu ndiye ________ wanga wabwino
dzina
anatsogolera
uthenga
Chivumbulutso 22:16 — “Ine Yesu, ndatuma mngelo wanga kuti achitire ________ uwu ku mipingo. Ine ndine Muzu ndi Chipatso cha Davide ndipo ndine Nthanda Yonyezimira.”
phokoso
umboni
njala
Mateyu 3:16 — Yesu atangobatizidwa, nthawi yomweyo potuluka mʼmadzi, kumwamba kunatsekuka ndipo taonani, Mzimu wa Mulungu anatsika ngati ________ natera pa Iye.
mkwati
nkhunda
kuchiritsa
Yohane 1:32 — Kenaka Yohane anapereka umboni uwu: “Ine ndinaona Mzimu Woyera ngati ________ kuchokera kumwamba nakhala pa Iye.
matenda
malonjezo
nkhunda
Mateyu 28:18 — Kenaka Yesu anabwera kwa iwo nati, “________ wonse kumwamba ndi dziko lapansi wapatsidwa kwa Ine.
umboni
mʼbado
Ulamuliro
Yohane 14:16 — Ine ndidzapempha Atate, ndipo adzakupatsani ________ ina kuti izikhala nanu nthawi zonse.
bwato
Nkhoswe
malungo
Aefeso 4:4 — Pali thupi limodzi ndiponso Mzimu mmodzi, monganso pali ________ chimodzi chimene anakuyitanirani.
chiyembekezo
chisomo
yekha
Ahebri 8:1 — Fundo yayikulu pa zimene tikunenazi ndi iyi: Tili naye ife Mkulu wa ansembe, amene anakhala ku dzanja lamanja la mpando ________ wa Mulungu Waulemerero kumwamba.
waufumu
analowa
manyazi
Ahebri 7:14 — Pakuti nʼzodziwika bwino kuti Ambuye athu anachokera fuko la ________. Kunena za fuko limeneli, Mose sananenepo kanthu za ansembe.
Olivi
Timoteyo
Yuda
Ahebri 4:14 — Popeza kuti tili ndi Mkulu wa ansembe wopambana, amene analowa kale kumwamba, Yesu Mwana wa Mulungu, tiyeni tigwiritsitse chikhulupiriro chathu chimene ________.
timavomereza
anagawikananso
chikhululukiro
Gawirani zotsatira zanu Ulalo wakopedwa Pitirizani Kuphunzira →
Kodi phunziroli lakuthandizani? Gawani umboni wanu waufupi kapena wathunthu — nkhani yanu imathandiza wina kupeza tsambali.
← Bwererani ku phunziroli